1 Akorinto 11:34 - Buku Lopatulika Ngati wina ali ndi njala adye kwao; kuti mungasonkhanire kwa chiweruziro. Koma zotsalazo ndidzafotokoza pakudza ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ngati wina ali ndi njala adye kwao; kuti mungasonkhanire kwa chiweruziro. Koma zotsalazo ndidzafotokoza pakudza ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngati wina ali ndi njala, ayambe wadya kwao, kuti Mulungu angakulangeni chifukwa cha kusonkhana kwanu. Koma zina zimene sindidatchule, ndidzazilongosola ndikabwera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati wina ali ndi njala, adye ku nyumba kwake kuti pamene musonkhana pamodzi zisafike poti muweruzidwe nazo. Ndipo ndikabwera ndidzakupatsani malangizo ena owonjezera. |
Koma za chopereka cha kwa oyera mtima, monga ndinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero chitani inunso.
Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine.
Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo mu Mipingo yonse.
Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi.
Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika mu Mipingo yonse.
Chifukwa cha ichi ndinakusiya iwe mu Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akulu m'midzi yonse, monga ndinakulamulira;