Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Akorinto 11:16 - Buku Lopatulika

Koma akaoneka wina ngati wotetana, tilibe makhalidwe otere, kapena ife, kapena Mpingo wa Mulungu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma akaoneka wina ngati wotetana, tilibe makhalidwe otere, kapena ife, kapena Mpingo wa Mulungu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono ngati wina afuna kutsutsapo pa zimenezi, ndingoti ife ndiponso mipingo ya Mulungu tilibe mwambo wina ai ndi womwewu basi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ngati wina akufuna kutsutsapo pa zimenezi, ife ndiponso mipingo ya Mulungu tilibe machitidwe ena apadera koma ndi omwewa.

Onani mutuwo



1 Akorinto 11:16
12 Mawu Ofanana  

Ndipo ndinatenga kalata yogulira, yina yosindikizidwa, monga mwa lamulo ndi mwambo, ndi yina yovundukuka;


ndipo anamva za iwe, kuti uphunzitsa Ayuda onse a kwa amitundu apatukane naye Mose, ndi kuti asadule ana ao, kapena asayende monga mwa miyambo.


amenewa uwatenge nudziyeretse nao pamodzi, nuwalipirire, kuti amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzachabe, koma kuti iwe wekhanso uyenda molunjika, nusunga chilamulo.


Koma ngati mkazi aweta tsitsi, kuli ulemerero kwa iye; pakuti tsitsi lake lapatsidwa kwa iye ngati chophimba.


Koma za chopereka cha kwa oyera mtima, monga ndinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero chitani inunso.


Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.


Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika mu Mipingo yonse.


Kodi sindine mfulu? Kodi sindine mtumwi? Kodi sindinaone Yesu Ambuye wathu? Kodi simuli inu ntchito yanga mwa Ambuye?


Kapena kodi ife tokha, Barnabasi ndi ine tilibe ulamuliro wakusagwira ntchito?


Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala mu Yudeya mwa Khristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa ndinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowa pa manja a Ayuda;