Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zao; ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa.
1 Akorinto 11:12 - Buku Lopatulika Pakuti monga mkazi ali wa kwa mwamuna, chomwechonso mwamuna ali mwa mkazi; koma zinthu zonse zili za kwa Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti monga mkazi ali wa kwa mwamuna, chomwechonso mwamuna ali mwa mkazi; koma zinthu zonse zili za kwa Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inde mkazi adapangidwa kuchokera kwa mwamuna, komanso tsopano mwamuna amabadwa mwa mkazi. Ndipo zinthu zonse zimachokera kwa Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti monga mkazi anachokera kwa mwamuna, momwemonso mwamuna anabadwa mwa mkazi. Koma zonse zichokera kwa Mulungu. |
Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zao; ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa.
Chifukwa zinthu zonse zichokera kwa Iye, zichitika mwa Iye, ndi kufikira kwa Iye. Kwa Iyeyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen.
koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse zili mwa Iye, ndi ife mwa Iye.
Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Khristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso;