koma mkazi chifukwa cha mwamuna; chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pake, chifukwa cha angelo.
1 Akorinto 11:11 - Buku Lopatulika Komanso mkazi sakhala wopanda mwamuna, kapena mwamuna wopanda mkazi, mwa Ambuye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Komanso mkazi sakhala wopanda mwamuna, kapena mwamuna wopanda mkazi, mwa Ambuye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe m'maso mwa Ambuye mkazi sali kanthu popanda mwamuna, ndiponso mwamuna sali kanthu popanda mkazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Komabe mwa Ambuye, mkazi amadalira mwamuna ndipo mwamuna amadalira mkazi. |
koma mkazi chifukwa cha mwamuna; chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pake, chifukwa cha angelo.
Pakuti monga mkazi ali wa kwa mwamuna, chomwechonso mwamuna ali mwa mkazi; koma zinthu zonse zili za kwa Mulungu.
Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.