Kwa Sara ndipo anati, Taona, ndapatsa mlongo wako ndalama zasiliva mazana khumi; taona, izo ndizo zoyeretsa maso za kwa onse amene ali ndi iwe: ndi pamaso pa onse ukhale wolungama.
1 Akorinto 11:10 - Buku Lopatulika koma mkazi chifukwa cha mwamuna; chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pake, chifukwa cha angelo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma mkazi chifukwa cha mwamuna; chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pake, chifukwa cha angelo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono, chifukwa cha angelo, mkazi azivala kanthu kumutu, kuti chikhale chizindikiro cha ulemu wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa chifukwa ichi, ndiponso pa chifukwa cha angelo, mkazi akuyenera kukhala ndi chizindikiro cha ulamuliro wake. |
Kwa Sara ndipo anati, Taona, ndapatsa mlongo wako ndalama zasiliva mazana khumi; taona, izo ndizo zoyeretsa maso za kwa onse amene ali ndi iwe: ndi pamaso pa onse ukhale wolungama.
Usalole m'kamwa mwako muchimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako chifukwa ninji, naononge ntchito ya manja ako?
Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.
Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?