monga inenso ndikondweretsa onse m'zinthu zonse, wosafuna chipindulo changa, koma cha unyunjiwo, kuti apulumutsidwe.
1 Akorinto 11:1 - Buku Lopatulika Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Khristu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Khristu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muzinditsanzira ine monga momwe inenso ndimatsanzira Khristu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsatirani chitsanzo changa, monga inenso nditsatira chitsanzo cha Khristu. |
monga inenso ndikondweretsa onse m'zinthu zonse, wosafuna chipindulo changa, koma cha unyunjiwo, kuti apulumutsidwe.
Abale, khalani pamodzi akutsanza anga, ndipo yang'anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife chitsanzo chanu.
Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m'mene mudalandira mauwo m'chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera;
si chifukwa tilibe ulamuliro, komatu kuti tidzipereke tokha tikhale kwa inu chitsanzo chanu, kuti mukatitsanze ife.
kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.