1 Akorinto 10:9 - Buku Lopatulika Kapena tisayese Ambuye, monga ena a iwo anayesa, naonongeka ndi njoka zija. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kapena tisayese Ambuye, monga ena a iwo anayesa, naonongeka ndi njoka zija. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tisapute Ambuye monga momwe adaaŵaputira ena mwa iwo: paja anthuwo adaphedwa ndi njoka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tisamuyese Khristu, monga ena mwa iwo anachitira ndipo anaphedwa ndi njoka. |
Pamenepo anthu anatsutsana ndi Mose, nati, Tipatseni madzi timwe. Koma Mose ananena nao, Mutsutsana nane bwanji? Muyeseranji Yehova?
Ndipo anatcha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, chifukwa cha kutsutsana kwa ana a Israele; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai?