1 Akorinto 10:5 - Buku Lopatulika Koma ochuluka a iwo Mulungu sanakondwere nao; pakuti anamwazika m'chipululu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ochuluka a iwo Mulungu sanakondwera nao; pakuti anamwazika m'chipululu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe ambirimbiri mwa iwo Mulungu sadakondwere nawo, kotero kuti adafera m'chipululu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale zinali choncho, Mulungu sanakondwere ndi ambiri a iwo, motero ambiri mwa iwo anafera mʼchipululu. |
Monga ndinaweruza makolo anu m'chipululu cha dziko la Ejipito, momwemo ndidzaweruza inu, ati Ambuye Yehova.
popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;
Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-Baranea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m'chigono, monga Yehova adawalumbirira.
Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adachimwawo, amene matupi ao adagwa m'chipululu?
Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale, kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, anaononganso iwo osakhulupirira.