1 Akorinto 10:15 - Buku Lopatulika Ndinena monga kwa anzeru; lingirirani inu chimene ndinena. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinena monga kwa anzeru; lingirirani inu chimene ndinena. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikulankhula nanu ngati anthu anzeru. Muweruze nokha zimene ndikunenazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikuyankhula kwa a anthu anzeru zawo, nokha muweruze pa zimene ndikunenazi. |
Chikho cha dalitso chimene tidalitsa, sichili chiyanjano cha mwazi wa Khristu kodi? Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Khristu kodi?
Abale, musakhale ana m'chidziwitso, koma m'choipa khalani makanda, koma m'chidziwitso akulu misinkhu.
Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.
Ndinena ichi kukuchititsani inu manyazi. Kodi nkutero kuti mwa inu palibe mmodzi wanzeru, amene adzakhoza kuweruza pa abale,
Koma za zoperekedwa nsembe kwa mafano: Tidziwa kuti tili nacho chidziwitso tonse. Chidziwitso chitukumula, koma chikondi chimangirira.