1 Akorinto 10:12 - Buku Lopatulika Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang'anire kuti angagwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang'anire kuti angagwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono amene akuganiza kuti waimirira molimba, achenjere kuti angagwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho, ngati mukuganiza kuti mwayima mwamphamvu, samalani mungagwe! |
Chifukwa chake yang'anirani mamvedwe anu; pakuti kudzapatsidwa kwa iye amene ali nacho; ndipo kwa iye amene alibe chidzachotsedwa, chingakhale chija aoneka ngati ali nacho.
Chabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi chikhulupiriro chako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu:
Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu;
Inu, tsono, okondedwa, pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osaweruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.