Ndipo analowa wina, nauza mbuye wake, kuti, Buthulo lofuma ku dziko la Israele lanena zakutizakuti.
1 Akorinto 1:26 - Buku Lopatulika Pakuti penyani maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iai; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti penyani maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iai; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abale, taganizani m'mene munaliri pamene Mulungu adakuitanani. Pakati panu panalibe ambiri amene anthu ankaŵayesa anzeru. Panalibenso ambiri amphamvu, kapena obadwa m'mabanja omveka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abale taganizirani mmene munalili musanayitanidwe. Si ambiri a inu munali a nzeru, si ambiri a inu munali a mphamvu zamakopedwe. Si ambiri a inu munali obadwa pa ulemerero. |
Ndipo analowa wina, nauza mbuye wake, kuti, Buthulo lofuma ku dziko la Israele lanena zakutizakuti.
Koma ndidzasiya pakati pako anthu ozunzika ndi osauka, ndipo iwo adzakhulupirira dzina la Yehova.
kuyambira pachiyambi, ndinayesa nkokoma inenso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira pachiyambi, kulembera kwa iwe tsatanetsatane, Teofilo wabwinotu iwe;
Nthawi yomweyo Iye anakondwera ndi Mzimu Woyera, nati, Ndikuvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda; indedi, Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu.
Pamenepo kazembe, pakuona chochitikacho anakhulupirira, nadabwa nacho chiphunzitso cha Ambuye.
ameneyo anali ndi kazembe Sergio Paulo, ndiye munthu wanzeru. Yemweyo anaitana Barnabasi ndi Saulo, nafunitsa kumva mau a Mulungu.
Koma ena anadziphatika kwa iye, nakhulupirira; mwa iwonso munali Dionizio Mwareopagi, ndi mkazi dzina lake Damarisi, ndi ena pamodzi nao.
Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitse nzeru ya dziko lapansi?
Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu.
imene saidziwa mmodzi wa akulu a nthawi ya pansi pano: pakuti akadadziwa sakadapachika Mbuye wa ulemerero;
Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?
Mkuluyo kwa mkazi womveka wosankhika, ndi ana ake, amene ine ndikondana nao m'choonadi; ndipo si ine ndekha, komanso onse akuzindikira choonadi;