Ndipo iye anapatsa chizindikiro tsiku lomwelo, nati, Chizindikiro chimene Yehova ananena ndi ichi, Taonani guwali la nsembe lidzang'ambika, ndi phulusa lili pa ilo lidzatayika.
1 Akorinto 1:22 - Buku Lopatulika Ndipo popeza Ayuda afunsa zizindikiro, ndi Agriki atsata nzeru: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo popeza Ayuda afunsa zizindikiro, ndi Agriki atsata nzeru: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ayuda amafuna kuwona zozizwitsa, pamene Agriki amafunafuna nzeru. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ayuda amafuna zizindikiro zodabwitsa ndipo Agriki amafunafuna nzeru, |
Ndipo iye anapatsa chizindikiro tsiku lomwelo, nati, Chizindikiro chimene Yehova ananena ndi ichi, Taonani guwali la nsembe lidzang'ambika, ndi phulusa lili pa ilo lidzatayika.
Ndipo Afarisi anatuluka, nayamba kufunsana naye, ndi kufuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba, namuyesa Iye.
Koma ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu.
Chifukwa chake Ayuda anayankha nati kwa Iye, Mutionetsera ife chizindikiro chanji, pakuti muchita izi?
Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikiro ndi zozizwa, simudzakhulupirira.