Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Akorinto 1:17 - Buku Lopatulika

Pakuti Khristu sananditume ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mau, kuti mtanda wa Khristu ungayesedwe wopanda pake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pakuti Khristu sanandituma ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mau, kuti mtanda wa Khristu ungayesedwe wopanda pake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Paja Khristu adandituma, osati kuti ndizibatiza ai, koma kuti ndizilalika Uthenga Wabwino. Ndipo ndiyenera kumaulalika mosagwiritsa ntchito luso lake la ulaliki, kuwopa kuti mtanda wa Khristu ungatheretu mphamvu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Pakuti Khristu sananditume ine kudzabatiza, koma kudzalalikira Uthenga Wabwino, osati ndi mawu anzeru za umunthu, kuopa kuti mtanda wa Khristu ungakhale wopanda mphamvu.

Onani mutuwo



1 Akorinto 1:17
13 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake pamene Ambuye anadziwa kuti Afarisi adamva kuti Yesu anayesa anthu ophunzira, nawabatiza koposa Yohane


(angakhale Yesu sanabatize yekha koma ophunzira ake),


Ndipo analamulira iwo abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Pamenepo anampempha iye atsotse masiku.


Ndipo ine, abale, m'mene ndinadza kwa inu, sindinadze ndi kuposa kwa mau, kapena kwa nzeru, polalikira kwa inu chinsinsi cha Mulungu.


Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu.


Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.


Pakuti, makalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mau ake ngachabe.


Ndipo ndingakhale ndili wosaphunzira m'manenedwe, koma sinditero m'chidziwitso, koma m'zonse tachionetsa kwa inu mwa anthu onse.


koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.


Pakuti sitinatsate miyambi yachabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu, koma tinapenya m'maso ukulu wake.