1 Akorinto 1:16 - Buku Lopatulika Koma ndinabatizanso a pa banja la Stefanasi; za ena, sindidziwa ngati ndinabatiza wina yense. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ndinabatizanso a pa banja la Stefanasi; za ena, sindidziwa ngati ndinabatiza wina yense. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inde ndidabatizanso Stefanasi ndi a m'banja mwake, koma sindikumbukira kuti pali winanso amene ndidamubatiza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Inde, ine ndinabatizanso a mʼbanja la Stefano, koma sindikumbukira ngati ndinabatizanso wina aliyense). |
Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.
Ndipo anawatenga ora lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yao; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pake.
Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefanasi, kuti ali chipatso choyamba cha Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),
Koma ndikondwera pa kudza kwao kwa Stefanasi, ndi Fortunato, ndi Akaiko; chifukwa iwo anandikwaniritsa chotsalira chanu.