Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

101 Mauvesi a M'Baibulo Okhudza Mowa

Ndikufuna ndikuuzani, mphamvu ya Yesu ikhoza kukuthandizani kugonjetsa chilichonse chomwe chikukuvutitsani. Iye anabwera kudzatipulumutsa, ndipo anagonjetsa mayesero onse popanda kuchimwa.

Nzeru zake zimatipatsa chikhululukiro, ndipo kuuka kwake kukuwonetsa kuti iye ndi wamphamvu kuposa imfa. Mulungu angakuchiritseni kuposa kungosiya kumwa mowa kapena zinthu zina zoipa; mphamvu yake ikhoza kuchotsa chizolowezi choipacho kotheratu.

Yesu anagonjetsa mdani ndipo ndi wokonzeka kukumasulani ku mavuto ndi imfa. Ingololani Mzimu Woyera akusinthe moyo wanu. Musamapeze zifukwa. Muli ndi mphamvu mwa Khristu yogonjetsa chilichonse.

Limbani mtima! Mudzakhala umboni wa mphamvu ya Yesu yosandutsa anthu.


Aefeso 5:18

Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:1

Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso m'goli la ukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 6:12

Zinthu zonse nzololedwa kwa ine, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwadi kwa ine, koma sindingalole kuti chilichonse chindigonjetse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 8:36

Tsono ngati Mwana akumasulani, mudzakhaladi mfulu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 6:10

mbala, aumbombo, zidakwa, augogodi, kapena achifwamba, ameneŵa sadzaulaŵa Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 20:1

Anthu okhuta vinyo amanyodola anzao, omwa zaukali amautsa phokoso. Aliyense wosokera nazo zimenezi ndi wopanda nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 9:20-21

Nowa anali mlimi ndipo anali woyamba kulima munda wamphesa.

Tsiku lina atangomwa vinyo, adaledzera, ndipo adavula zovala zake zonse, nakagona ali maliseche m'hema mwake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 1:9

Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 4:7

Tsono muzigonjera Mulungu. Satana muzilimbana naye, ndipo adzakuthaŵani.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:8

Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 19:32-35

Tiye tiŵaledzeretse abamboŵa kuti agone nafe, kuti mtundu usathe.

Choncho usiku womwewo anawo adampatsa vinyo bambo waoyo. Zitatero, mwana wamkuluyo adagona ndi bambo wake. Pamenepo nkuti bamboyo ataledzera kwambiri, kotero kuti sankadziŵa zimene zinkachitika.”

M'maŵa mwake mwana wamkuluyo adauza mng'ono wake uja kuti, “Ine dzulo ndidagona ndi atate. Tiye tsono tiŵaledzeretsenso kuti iwenso ugone nawo, kuti choncho mtundu wathu usathe.”

Motero usiku umenewo adamledzeretsanso, ndipo mwana wamng'onoyo adagona ndi bambo wake. Nthaŵi imeneyinso nkuti bamboyo ataledzera, kotero kuti sadadziŵe zochitikazo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 10:13

Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 14:21

Nkwabwino kusadya nyama, kusamwa vinyo, ndiponso kusachita kanthu kalikonse kamene kangachimwitse mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 20:5

Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 26:41

Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 10:9

“Usamwe vinyo kapena chakumwa china champhamvu, iwe ndi ana ako uli nawoŵa, pamene mukupita ku chihema chamsonkhano, kuwopa kuti mungafe. Limeneli likhale lamulo losatha pa mibadwo yanu yonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 6:5-6

Ngati takhala amodzi ndi Khristu mu imfa yake, momwemonso tidzakhala amodzi naye pa kuuka kwa akufa, monga momwe adaukira Iyeyo.

Tidziŵa kuti mkhalidwe wathu wakale udapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kuti khumbo lathu lokonda machimo liwonongeke, ndipo tisakhalenso akapolo a uchimo.

Mutu    |  Mabaibulo
Tito 2:11-12

Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse.

Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Numeri 6:3

asamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa. Asamwe vinyo wopangidwa ndi mphesa kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo asamwe madzi amphesa kapena kudya mphesa zaziŵisi kapena zouma.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 29:6

Munalibe buledi woti muzidya, ngakhalenso vinyo kapena chakumwa chaukali, koma Chauta adakupatsani zonse zokusoŵani, kuti mudziŵe kuti Iye ndi Chauta, Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Oweruza 13:4

Ndiye inu mudzisamale bwino, musamamwe vinyo kapena chakumwa china choledzeretsa, ndipo musamadye chakudya chilichonse chosaloledwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Oweruza 13:7

Koma anandiwuza kuti, ‘Mudzakhala ndi pathupi ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Ndiye musamamwe vinyo kapena chakumwa china choledzeretsa, ndipo musamadye chakudya chosaloledwa chilichonse, chifukwa mnyamatayo adzakhala Mnaziri, wopatulikira Mulungu, kuyambira tsiku la kubadwa kwake mpaka tsiku la kufa kwake.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 1:14-15

Tsono adamufunsa kuti, “Mai, kodi mukhala chiledzerere mpaka liti? Pitani, akayambe watha vinyo mwamwayu.”

Koma Hana adayankha kuti, “Iyai mbuyanga, sindidamwe vinyo kapena chakumwa chaukali chilichonse. Munthune ndili ndi chisoni choopsa. Ndakhala ndikulira kwa Chauta chifukwa cha chisoni changachi.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 11:13

Davide adaitana Uriya, nadya naye ndipo adamwa kwambiri, kotero kuti Davide adamledzeretsa. Komabe madzulo Uriya adapita kukagona pogona pake, pamodzi ndi antchito a mfumu, osapita kunyumba kwake.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 13:28

Tsono Abisalomu adalamula antchito ake kuti, “Muwonetsetse nthaŵi imene Aminoni akhale ataledzera ndi vinyo. Ndikakuuzani kuti, ‘Kanthani Aminoni!’ Pomwepo mumuphe. Musaope, nanga sindine ndakulamulani? Mulimbe mtima, ndipo muchite chamuna.”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 16:9

Tsono munthu wina dzina lake Zimuri, amene anali mkulu woyang'anira hafu la magaleta ake, adamchita chiwembu. Pamene Elayo anali ku Tiriza, namamwa mpaka kuledzera m'nyumba ya Ariza, amene ankayang'anira nyumba yachifumu ku Tirizako,

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 20:16

Adatuluka masana nthaŵi imene Benihadadi ndi mafumu 32 othandizana nawo aja ankamwa mpaka kuledzera m'mahema mwao.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 12:39-40

Ndipo adakhala komweko masiku atatu pamodzi ndi Davide namadya zimene abale ao anali ataŵakonzekera.

ndi Isimaya wa ku Gibiyoni, amene anali wamphamvu mwa anthu makumi atatu aja ndiponso mmodzi mwa atsogoleri ao. Panalinso Yeremiya, Yahaziele, Yohanani, Yozabadi wa ku Gedera,

Nawonso anansi ao, ochokera ngakhale ku Isakara ndi Zebuloni ndi Nafutali, adadza atasenzetsa chakudya abulu ao, ngamira zao, nyulu zao ndi ng'ombe zao. Adazisenzetsa chakudya chambiri, makeke ankhuyu, ntchichi zamphesa, vinyo ndiponso mafuta. Adabweranso ndi ng'ombe ndi nkhosa zambiri, poti ku dziko la Israele kunali chisangalalo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 75:8

M'manja mwa Chauta mulitu chikho cha vinyo wofanizira chilango chake, vinyo wotutuma ndi wothirako dzoŵaŵa. Adzatsanyula vinyoyo, ndipo oipa onse a pa dziko lapansi adzamwa, nadzagugudiza mpaka ndungundungu zake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 104:15

Amapezamo vinyo wosangalatsa mtima wake, mafuta odzola kuti thupi lake lisisire, ndiponso buledi kuti ampatse mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 4:17

Paja kuchita zoipa ndiye chakudya chao, kuchita ndeu ndiye chakumwa chao.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 21:17

Amene amakondetsa zosangalatsa, adzasanduka munthu wosauka. Amene amakondetsa vinyo ndi mafuta, sadzalemera.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 23:19-20

Mwana wanga, tamvera, ndipo ukhale wanzeru, mtima wako uuyendetse m'njira yabwino.

Ngati ndiwe munthu wadyera, udziletse kuti usachite khwinthi.

Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera, kapena pakati pa anthu odya nyama mwadyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 23:29-30

Ndani ali ndi tsoka? Ndani ali ndi chisoni? Ndani ali pa mkangano? Ndani akudandaula? Ndani ali ndi zilonda zosadziŵika magwero ake? Ndani ali wofiira maso?

Usasirire zakudya zake zokoma, poti zimenezi ndi zakudya zonyenga.

Ndi amene amakhalitsa pamene pali vinyo, amene amamwa nawo vinyo wosanganiza ndi zina.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 23:31-32

Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo, pamene akututuma m'chikho namakoma poloŵa ku m'mero.

Potsiriza pake amaluma ngati njoka, ndipo amanjenjedula ngati mphiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 31:4

Iwe Lemuwele, mafumu sayenera kumamwa vinyo, olamulira asamalakalaka zakumwa zaukali,

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 31:5-7

kuwopa kuti angaiŵale malamulo a dziko, ndi kukhotetsa zinthu zoyenerera anthu osauka.

Munthu amene ali pafupi kufa, uzimpatsa chakumwa chaukali, ndipo munthu amene ali pa mavuto oopsa, uzimpatsa vinyo.

Amwe kuti aiŵale umphaŵi wake asakumbukirenso kuvutika kwake.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 2:3

Potsata nzeruzo ndidaayesa kudzisangalatsa ndi vinyo, koma umenewo unali uchitsiru. Ndinkati mwina kapena njira yotere nkukhala yopambana, imene anthu amatsata pofuna kusangalala pa masiku oŵerengeka a moyo wao.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 9:7

Ndiye iwe usaope, uzidya chakudya chako mokondwa, uzimwa vinyo wako ndi mtima wosangalala, pakuti Mulungu wavomereza kale zochita zakozo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 5:11

Tsoka kwa amene amadzuka m'mamaŵa nathamangira chakumwa choledzeretsa, amene amamwa mpaka usiku kufikira ataledzera kotheratu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 5:22

Tsoka kwa zidakwa zimene zimaika mtima pa vinyo! Tsoka kwa anthu amene saopa konse kusakaniza zakumwa zaukali!

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 24:9

Anthu saimbanso pomwa vinyo, akamamwa zaukali zimaŵaŵa m'kamwa mwao.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 28:1

Tsoka kwa ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efuremu! Tsoka kwa ulemerero wake umene wayamba kufota ngati duŵa, mzinda uja uli kumtunda kwa chigwa chachonde, umene amanyadira anthu oledzera vinyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 28:7

Nawonso aŵa ali punzipunzi chifukwa cha vinyo, akudzandira ndi zakumwa zaukali. Ansembe ndi aneneri ali punzipunzi ndi zakumwa zaukali. Onsewo ndi osokonezeka chifukwa cha vinyo, ali dzandidzandi chifukwa cha zakumwa zaukali. Amamvetsa molakwa zimene amaziwona m'masomphenya, amalephera kuweruza milandu imene amadzaŵatulira.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 56:12

Zidakwa zimenezi zimati, ‘Tiyeni timwe vinyo, tiyeni timwe zakumwa zamphamvu mpaka kukhuta. Maŵa lidzakhala ngati leroli, mwina mwake nkudzaposa lero limene.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 35:5-6

Tsono ndidaika mbiya zodzaza ndi vinyo ndi zikho zomwera pamaso pa Arekabuwo, ndipo ndidaŵauza kuti, “Nayu vinyo, imwani.”

Koma iwowo adati, “Ife sitimwa vinyoyu, poti kholo lathu Yonadabu mwana wa Rekabu adatilamula kuti, ‘Musadzamwe vinyo, inuyo ndi ana anu omwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 44:21

Wansembe asamwe vinyo pamene ali pafupi kuloŵa m'bwalo lam'kati.

Mutu    |  Mabaibulo
Hoseya 4:11

Chauta akuti, “Vinyo, kaya ndi wakale kaya ndi watsopano, amaononga nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoweli 1:5

Dzukani inu zidakwa, ndipo mulire. Mulire modandaula inu nonse okonda vinyo: mphesa zotchezera vinyo watsopano zaonongedwa,

Mutu    |  Mabaibulo
Amosi 2:8

Anthuwo amagona pambali pa malo aliwonse opembedzerapo, pa zovala zimene adalandira kwa osauka ngati chikole. M'nyumba ya Mulungu amamweramo zakumwa za anthu amene adaŵalipitsa pa mlandu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 2:11

Munthu wina atamapita uku ndi uku akulalika zabodza kuti, ‘Ndithudi mudzakhala ndi vinyo ndi zakumwa zamphamvu zambiri,’ mlaliki wotere ndi amene anthu aŵa angamkonde.

Mutu    |  Mabaibulo
Habakuku 2:5

Monga munthu wokhuta vinyo ali wosokonezeka, chonchonso munthu wodzitama ndi wosakhazikika. Ndi waumbombo kwambiri ngati manda, ngati imfa amakhala wosakhuta. Amagwira anthu a mitundu yonse, amaŵasonkhanitsa ngati ake.”

Mutu    |  Mabaibulo
Habakuku 2:15

Tsoka kwa amene amamwetsa anzake zaukali, amene amaŵaledzeretsa kuti aŵachititse manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 11:18-19

Paja Yohane Mbatizi atabwera, ankasala zakudya ndi zakumwa, anthu nkumati, ‘Adagwidwa ndi mzimu woipa.’

Mwana wa Munthu adabwera nkumadya ndi kumwa ndithu, anthu amvekere, ‘Tamuwonani, munthuyu ndi wadyera, chidakwa, ndiponso bwenzi la anthu amsonkho ndi anthu osasamala Malamulo.’ Komabe chilungamo cha nzeru za Mulungu chimatsimikizika ndi zochita zake.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 24:49

Ndiye adzayamba kumenya antchito anzake, ndiponso kumadya ndi kumamwa pamodzi ndi zidakwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 1:15

popeza kuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Sazidzamwa konse vinyo kapena choledzeretsa china chilichonse. Adzakhala wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ngakhale asanabadwe nkomwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 7:33-34

“Paja Yohane Mbatizi atabwera, ankasala zakudya ndipo sankamwa vinyo, inu nkumati, ‘Adagwidwa ndi mizimu yoipa.’

Mwana wa Munthu adabwera, nkumadya ndi kumwa ndithu, inu mumvekere, ‘Tamuwonani, munthuyu ndi wadyera, chidakwa, ndiponso bwenzi la anthu amsonkho ndi anthu osasamala Malamulo.’

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 10:34

Adabwera kwa wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuŵamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 12:45

“Koma ngati ndi wantchito woipa, mumtima mwake azidzati, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera.’ Ndiye adzayamba kumenya antchito anzake, amuna ndi akazi, ndiponso kumadya, kumamwa ndi kuledzera.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 13:13

Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 5:11

Koma ndidaakulemberani kuti musamayanjane ndi munthu amene amati ndi mkhristu, pamene chikhalirecho ndi munthu wadama, kapena waumbombo, wopembedza mafano, waugogodi, chidakwa, kapena wachifwamba. Munthu wotere musamadye naye nkomwe.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 10:31

Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:19-21

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa,

Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai.

kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,

dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:5

Kufatsa kwanu kuziwoneka pamaso pa anthu onse. Ambuyetu ali pafupi.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 2:16

Wina aliyense asakuzengeni mlandu pa nkhani yokhudza zakudya kapena zakumwa, kapena pa zokhudza masiku a chikondwerero, kapena a mwezi wokhala chatsopano, kapena pa zokhudza tsiku la Sabata.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 5:6-8

Nchifukwa chake tsono tisagone tulo monga momwe amachitira anthu ena, ife tikhale maso, tikhale osaledzera.

Anthu ogona tulo, amagona usiku, anthu oledzera amaledzera usiku.

Koma ife, popeza kuti zathu nzausana, tisamaledzera. Tikhale titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala chachitsulo chapachifuwa. Ndipo ngati chisoti choteteza kumutu tivale chiyembekezo chakuti tidzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 3:2-3

Woyang'anira Mpingo azikhala munthu wopanda chokayikitsa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, akhale wodzigwira, wa maganizo anzeru, waulemu, wosamala bwino alendo, ndi wotha kuphunzitsa.

Asakhale chidakwa, asakhale wandeu, koma wofatsa, wosakangana ndi anthu, ndi wosakonda ndalama.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 3:8

Chimodzimodzinso ndi atumiki a mpingo: akhale ochita zachiukulu, osanena paŵiripaŵiri, osakhala ozoloŵera zoledzeretsa, osakonda udyo phindu la ndalama.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 5:23

Uleke kumangomwa madzi okha. Koma uzimwako vinyo pang'ono, paja umavutika ndi m'mimba, ndiponso chifukwa cha kudwaladwala kwako kuja.

Mutu    |  Mabaibulo
Tito 1:7

Woyang'anira mpingo azikhala wosapalamula konse, chifukwa ali ngati kapitao m'banja la Mulungu. Asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena chidakwa, kapena wandeu, kapenanso wokonda kudya phindu la ndalama.

Mutu    |  Mabaibulo
Tito 2:3

Chimodzimodzinso azimai achikulire, uŵauze kuti azikhala ndi makhalidwe oyenera azimai oyera mtima. Asakhale osinjirira anzao kapena akapolo a zoledzeretsa. Akhale alangizi abwino,

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 1:13

Nchifukwa chake mtima wanu ukhale wokonzeka. Khalani tchelu. Khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa kukoma mtima kwa Mulungu pamene Yesu Khristu adzaoneke.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 4:3

Paja kale mudakhala mukutaya nthaŵi yochuluka pakuchita zinthu zimene akunja amazikonda. Munkatsata zonyansa, zilakolako zoipa, kuledzera, dyera, maphokoso apamoŵa, ndi kupembedza mafano konyansa.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 32:33

ndi oipa kwambiri ngati vinyo wosanganiza ndi ululu wa njoka, ululu wopweteka wa mphiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 19:14

Chauta waŵasokoneza Aejipito. Iwo akuchita dzandidzandi pa ntchito zao zonse, ngati chidakwa choterereka pa masanzi ake omwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 60:3

Inu mwalola anthu anu kuti aone mavuto aakulu. Mwatipatsa vinyo wachilango kuti timwe, ndipo tikudzandira naye.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 25:27

“Kenaka udzaŵauze kuti, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Imwani, muledzere, musanze, mugwe osadzukanso, chifukwa cha nkhondo imene ndikutumiza pakati panu.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 31:6

Munthu amene ali pafupi kufa, uzimpatsa chakumwa chaukali, ndipo munthu amene ali pa mavuto oopsa, uzimpatsa vinyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 107:27

Adachita chizungulire namadzandira ngati anthu oledzera, kenaka nkuthedwa nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 29:9

Mudodome ndipo mukhale ozizwa. Dzichititseni khungu ndipo mukhalebe osapenya. Muledzere, koma osati ndi vinyo, ndipo mudzandire, koma osati ndi chakumwa chaukali.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 1:15

Koma Hana adayankha kuti, “Iyai mbuyanga, sindidamwe vinyo kapena chakumwa chaukali chilichonse. Munthune ndili ndi chisoni choopsa. Ndakhala ndikulira kwa Chauta chifukwa cha chisoni changachi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 12:25

Iwowo amanka nafufuza njira mumdima mopanda kuŵala, nkumayenda ali dzandidzandi ngati oledzera.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 5:22-23

Tsoka kwa zidakwa zimene zimaika mtima pa vinyo! Tsoka kwa anthu amene saopa konse kusakaniza zakumwa zaukali!

Amalungamitsa wolakwa chifukwa cha chiphuphu nkuipitsa mlandu wa munthu wosalakwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 69:12

Anthu okhala pa chipata amandinena, ndipo zidakwa zimandiimba nyimbo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 31:6-7

Munthu amene ali pafupi kufa, uzimpatsa chakumwa chaukali, ndipo munthu amene ali pa mavuto oopsa, uzimpatsa vinyo.

Amwe kuti aiŵale umphaŵi wake asakumbukirenso kuvutika kwake.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 24:48-49

Koma ngati ndi wantchito woipa, mumtima mwake azidzati, ‘Mbuye wanga akuchedwa.’

Ndiye adzayamba kumenya antchito anzake, ndiponso kumadya ndi kumamwa pamodzi ndi zidakwa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 9:27

Ndimazunza thupi langa ndi kuligonjetsa, kuti likhale ngati kapolo wondimvera. Ndimachita zimenezi kuwopa kuti ine ndemwe, amene ndidaitana ena ku mpikisano, ndingapezeke wosayenera kuchita nao mpikisanowo.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 5:15-18

Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru.

Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa.

Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵani zimene Ambuye afuna kuti muchite.

Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 4:16

Udziyang'anire bwino wekha, ndi kusamala zimene umaphunzitsa. Ulimbikire kutero, chifukwa pakuchita zimenezi udzadzipulumutsa iwe wemwe, ndiponso anthu amene amamva mau ako.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 8:9

Komabe chenjerani kuti ufulu wanuwu pochita zinthu, ungaphunthwitse ena amene chikhulupiriro chao nchosalimba kwenikweni.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 21:34

“Chenjerani kuti mitima yanu ingapusitsidwe ndi maphwando, kuledzera, ndi kudera nkhaŵa za moyo uno, kuti tsikulo lingakufikireni modzidzimutsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 16:5-6

Chauta ndiye chuma changa ndi choloŵa changa. Tsogolo langa lili m'manja mwanu.

Malire a malo anga andikhalira mwabwino. Inde, ndalandira madalitso abwino ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 23:5

Inu mumandikonzera chakudya, adani anga akuwona. Mumandilandira bwino podzoza mutu wanga ndi mafuta, mumadzaza chikho changa mpaka kusefukira.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 10:17

Koma ndiwe wodala iwe dziko, ngati mfumu yako ndi mwana wa mfulu. Ndiwe wodala ngati nduna zako zimachita phwando pa nthaŵi yabwino, kuti zikhale zamphamvu, osati kuti ziledzere.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 22:18

Ndithu ndikunenetsa kuti kuyambira tsopano sindidzamwanso konse chakumwa cha mtengo wamphesa, mpaka Mulungu atadzakhazikitsa ufumu wake.”

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga wamuyaya, Mwini wapadziko lonse! Ndikukutamandani chifukwa ndinu Wolungama, Woyera, woyenera kutamandidwa ndi kupembedzedwa kopambana. Atate, ndikupempha kwa inu Mulungu wanga wakumwamba, chifukwa ndinu nokha muli ndi mphamvu zomasula ndi kukonzanso moyo wanga. Mawu anu amati: "Ngati Mwana adzakumasulani, mudzakhala mfulu ndithu." Ndikukupemphani kuti muphwanye unyolo uliwonse womwe ukundimanga ku mowa. Ndithandizeni kulimbitsa chikhulupiriro changa ndi kukhala wolimba polimbana ndi chiyeso cha mowa, ndi thandizo la Mzimu Woyera wanu. Ndithandizeni kusiya choipachi kuti ndibwezeretse thanzi langa, chuma changa ndi banja langa, ndikufuna kuyenda monga mwa chifuniro chanu, chifukwa mawu anu amanenadi kuti: "Akuba, osirira, oledzera, otemberera, ndi achinyengo sadzalowa Ufumu wa Mulungu." Ndidziwitseni kukhala moyo wokondweretsa inu ndi onse oyandikira nane, sindikufunanso kupatsa mdani malo m'moyo wanga. Ndisungeni ndi kuwafalitsa onse omwe mwanjira ina akufuna kundigwetsa mu mowa. Ambuye, ndikupemphaninso kuti mumasule ndi kukonzanso miyoyo ya anthu omwe akukumana ndi vuto lomweli, awatsogolereni, awathandizeni ndipo amvetsetse kuti mwa inu nokha mupeza ufulu weniweni wakuthupi ndi wauzimu, ndipo kuti pogwirana chanza nanu pokha tingathe kugonjetsa chizolowezi chilichonse, chifukwa ndinu nokha wopereka chigonjetso. M'dzina la Yesu. Ameni.