Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa

Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano


Masalimo 150 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika
Masalimo 150

Zolengedwa zonse zilemekeze Mulungu

1 Aleluya. Lemekezani Mulungu m'malo ake oyera; mlemekezeni m'thambo la mphamvu yake.

2 Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba; mlemekezeni monga mwa ukulu wake waunjinji.

3 Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga; mlemekezeni ndi chisakasa ndi zeze.

4 Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang'ombe: Mlemekezeni ndi zoimbira za zingwe ndi chitoliro.

5 Mlemekezeni ndi nsanje zomveka: Mlemekezeni ndi nsanje zoliritsa.

6 Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Aleluya.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi