Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa

Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano


Masalimo 133 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika
Masalimo 133

Chikondano cha abale ndi chokoma
Nyimbo yokwerera; ya Davide.

1 Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!

2 Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake.

3 Ngati mame a ku Heremoni, akutsikira pa mapiri a Ziyoni. Pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo, ndilo moyo womka muyaya.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi