Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa

Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano


Masalimo 129 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika
Masalimo 129

Israele asautsidwa koma osafafanizidwa
Nyimbo yokwerera.

1 Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga, anene tsono Israele;

2 Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga; koma sanandilake.

3 Olima analima pamsana panga; anatalikitsa mipere yao.

4 Yehova ndiye wolungama; anadulatu zingwe za oipa.

5 Achite manyazi nabwerere m'mbuyo. Onse akudana naye Ziyoni.

6 Akhale ngati udzu womera patsindwi, wakufota asanauzule;

7 umene womweta sadzaza nao dzanja lake, kapena womanga mitolo sakupatira manja.

8 Angakhale opitirirapo sanena, Dalitso la Mulungu likhale pa inu; tikudalitsani m'dzina la Yehova.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi