Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa

Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano


Masalimo 126 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika
Masalimo 126

Ayamikira mokondwerera kuti Mulungu anabweza ukapolo wao
Nyimbo yokwerera.

1 Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni, tinakhala ngati anthu akulota.

2 Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, ndi lilime lathu linafuula mokondwera; pamenepo anati kwa amitundu, Yehova anawachitira iwo zazikulu.

3 Yehova anatichitira ife zazikulu; potero tikhala okondwera.

4 Bwezani ukapolo wathu, Yehova, ngati mitsinje ya kumwera.

5 Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera.

6 Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi