Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa

Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano


1 Samueli 31 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika
1 Samueli 31

Saulo ndi ana ake atatu aphedwa ndi Afilisti pa Gilibowa
( 1Mbi. 10.1-12 )

1 Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisraele; Aisraele nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m'phiri la Gilibowa.

2 Ndipo Afilisti anapirikitsa, osawaleka Saulo ndi ana ake; ndipo Afilisti anapha Yonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisuwa, ana a Saulo.

3 Ndipo nkhondoyo inamkulira Saulo kwambiri, oponya mivi nampeza; ndipo iye anasautsika kwakukulu chifukwa cha oponya miviyo.

4 Tsono Saulo ananena ndi wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana; chifukwa anaopa ndithu. Chifukwa chake Saulo anatenga lupanga lake naligwera.

5 Ndipo pakuona kuti Saulo anafa, wonyamula zida zake yemwe, anagwera lupanga lake, nafera limodzi ndi iye.

6 Chomwecho adamwalira pamodzi Saulo ndi ana ake atatu, ndi wonyamula zida zake, ndi anthu ake onse, tsiku lomwe lija.

7 Ndipo pamene Aisraele akukhala tsidya lina la chigwa, ndi iwo akukhala tsidya la Yordani, anaona kuti Aisraele alikuthawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake anafa, iwowa anasiya mizinda yao, nathawa; ndipo Afilisti anadza nakhala m'menemo.

8 Ndipo kunali m'mawa mwake, pakubwera Afilisti kuvula akufawo, anapeza Saulo ndi ana ake atatu ali akufa m'phiri la Gilibowa.

9 Ndipo anadula mutu wake, natenga zida zake, natumiza m'dziko lonse la Afilisti mithenga yolalikira kunyumba ya milungu yao, ndi kwa anthu.

10 Ndipo anaika zida zake m'nyumba ya Asitaroti; napachika mtembo wake ku linga la ku Beteseani.

11 Koma pamene a ku Yabesi-Giliyadi anamva zimene Afilisti anamchitira Saulo,

12 ngwazi zonse zinanyamuka ndi kuchezera usiku kuyenda, natenga mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, pa linga la Beteseani; nafika ku Yabesi-Giliyadi naitentha kumeneko.

13 Natenga mafupa ao nawaika patsinde pa mtengo wa bwemba uli mu Yabesi, nasala kudya masiku asanu ndi awiri.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi