2 nilakukoma pakuyima kwalene, chikondwelelo chadziko lentse lapantsi. Phili la Ziyoni, chakudzulu, guta la mambo nkulu.
Ngaadalisiwe Chawuta kuchoka mu Ziyoni, uyo an'khala mu Jerusalema. Aleluya!
Mulungu aniyetima kuchoka paphili la Ziyoni, phili labwino kwene-kwene.
Jese lake lili mu Salemu, mbuto yake yakukhala ili mu Ziyoni.
Bzinthu bzakulemekezeka bzikulewedwa padzulu pako, iwe guta la Mulungu. Selah.
Kuzani Chawuta Mulungu wathu! Kotamilani paphili lake lakuyela; pakuti Chawuta Mulungu wathu niwakuyela!