14 pakuti uyu ni Mulungu wathu, kufika lini nalini, an'zatitsogolela kufika kufa.
Ine ninti kwa Chawuta, “Ndimwe Mfumu wangu, ndilibe chabwino kunja kwayimwe.”
An'tsogolela wakubzichepesa kulinganiza, anfundisa wakubzichepesa njila yake.
Koma ine nin'themba imwe, Chawuta, ndiniti, “Ndimwe Mulungu wangu.”
Kufikila ndakalamba, kufikila ndachena nsolo, imwe Mulungu lekani kundisiya! Kufikila ndalalikila bzamphamvu zanu kum'badwe unango, mphamvu zanu, kwawentse am'bwela.
Munin'tsogolela namalango yanu, pakumalizila muchizanditambila nambili.
Thupi langu nankhumbukila zangu bzingataze, koma Mulungu ndiye mwala wantima wangu nachigawo changu kufika lini nalini.