4 Pitani pamisuwo yake nakutenda! Namubzintalo bzake nadumbizo! Pelekani kutenda kwayiye, dalisani dzina lake!
Nzayo zathu zayima, pamisuwo yako, iwe Jerusalema!
uko kunkwila mishowo, mishowo ya Chawuta; ninga umboni kwa Izraeli, kuti atende dzina la Chawuta.
Imwe Mulungu, dumbizo linkomela imwe mu Ziyoni, pomwe malumbilo yathu yan'dzadzikiziwa kwayimwe.
Nin'zabwela munyumba yanu nantsembe zakutentha, ndichichita bzandidalumbila.
Tiyendeni pamaso pake nakutenda! Tichite chiwowo chakukondwa nanyimbo zakudumbiza!
Imbilani Chawuta, dalisani dzina lake! Lalikilani chipulumuso chake ntsiku nantsiku!
Pelekani kwa Chawuta mbili yadzina lake, takulani mpfupo mubwelese kubzintalo bzake!
Lekani adumbize dzina lanu likulu lin'gopsa! Iye niwakuyela!