4 Ng'ombe zakuyipa, zakuwonda zile zidadya zabwino, zakunenepa zinomwe. Pamwepo Farawo adalamuka.
Pamwepo adawona ng'ombe zinomwe zikazi zabwino zakunenepa, zichibula m'madzi zichidya mumitete.
Adazawona pomwe ng'ombe zikazi zinomwe zakuyipa zakuwonda zichibula mu Nayilo zichikayima pakhana ng'ombe zile zikazi zakunenepa, mphepete mwakamadzi.
Adagona pomwe nkulota kachiwili; adalota ngala zinomwe zatiligu zakukhuma, zabwino zikhali patsinde ibodzi.