8 Tsapano mwanangu, unditetekele bzandikukuwuza kuti uchite.
Chawuta adati kwayiye, “M'mimba mwako muna mishowo miwili, wanthu awili, wawun'zabala an'zakhala wakugawika. Munango an'zakhala wamphamvu kuposa munango, nkulu an'zatumikila mung'ono.”
Koma amayi wake adati, “Mwanangu, tembelelo limwelo ngalibwele kwayine, iwe yenda ukachite bzandakuwuza.”
Tsapano mwanangu, tetekela bzandikukuwuza. Iwe uthawile ku Harani kwamano wangu Labhani,
‘Ndibweleseleko nyama yan'thengo undiphikile chakudya chabwino, ndikadya ndichizakudalisa patsogolo pa Chawuta ndinati ndafa.’
Yenda kuthanga undibwelesele tuwana twambuzi tuwili twakunenepa, ndizaphikile apayi wako chakudya chabwino chaanfunisisa.